Wolembedwa na Mateyo 6:1-34

  • ULALIKI WA PA PHILI (1-34)

    • Pewani kucita zabwino modzionetsela (1-4)

    • Mmene tingapemphelele (5-15)

      • Pemphelo la citsanzo (9-13)

    • Kusala kudya (16-18)

    • Cuma padziko lapansi komanso kumwamba (19-24)

    • Lekani kuda nkhawa (25-34)

      • Pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba (33)

6  “Samalani kuti musamacite zabwino* pamaso pa anthu kuti akuoneni, cifukwa mukatelo simudzalandila mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba.  Conco pamene mukupeleka mphatso za cifundo,* musamalize lipenga mmene amacitila anthu acinyengo m’masunagoge na m’misewu, kuti anthu awatamande. Ndithu nikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yawo yonse.  Koma inu mukamapeleka mphatso za cifundo, musalole kuti dzanja lanu lamanzele lidziŵe zimene dzanja lanu lamanja likucita,  kuti mphatso zanu za cifundo zikhale zamseli. Mukatelo, Atate wanu amene amaona ali kosaoneka adzakudalitsani.  “Komanso mukamapemphela, musamacite mmene anthu acinyengo amacitila, cifukwa iwo amakonda kupemphela ataimilila m’masunagoge na pa mphambano za misewu ikulu-ikulu kuti anthu awaone. Ndithu nikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yawo yonse.  Koma iwe ukafuna kupemphela, uziloŵa m’cipinda cako kwawekha ndipo uzipemphela kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatelo, Atate wako amene amaona ali kosaonekako adzakudalitsa.  Popemphela, usamanene mawu amodzi na amodzi, mmene amacitila anthu amitundu ina, cifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu adzawamvela akaculukitsa mawu.  Conco musakhale ngati iwo cifukwa Atate wanu amadziŵa zimene mukufunikila ngakhale musanam’pemphe n’komwe.  “Koma inu muzipemphela motele: “‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.* 10  Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba cimodzimodzinso pansi pano. 11  Mutipatse cakudya cathu ca lelo, 12  ndipo mutikhululukile macimo athu* mmenenso ife takhululukila amene anatilakwila.* 13  Ndiponso musatiloŵetse m’mayeselo, koma mutilanditse* kwa woipayo.’ 14  “Pakuti mukamakhululukila anthu zolakwa zawo, nayenso Atate wanu wa kumwamba adzakukhululukilani. 15  Koma ngati simukhululukila anthu zolakwa zawo, nayenso Atate wanu sadzakukhululukilani zolakwa zanu. 16  “Mukamasala kudya, lekani kuonetsa nkhope zacisoni, monga mmene acinyengo aja amacitila. Pakuti iwo amaipitsa nkhope zawo* kuti aonekele kwa anthu kuti akusala kudya. Ndithu nikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yawo yonse. 17  Koma iwe ukamasala kudya, uzidzola mafuta kumutu na kusamba kumaso 18  kuti usaonekele kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate wako yekhayo amene ali kosaoneka. Ukatelo, Atate wako amene amaona ali kosaonekako adzakudalitsa. 19  “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi pamene njenjete na nguwe zimawononga, komanso pomwe mbala zimathyola na kuba. 20  Koma mudziunjikile cuma kumwamba, kumene njenjete na nguwe siziwononga, komanso kumene mbala sizithyola na kuba. 21  Pakuti kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko. 22  “Nyale ya thupi ni diso. Conco, ngati diso lako ni lolunjika pa cinthu cimodzi,* thupi lako lonse lidzawala. 23  Koma ngati diso lako ni la dyela,* thupi lako lonse lidzacita mdima. Ngati kuwala kuli mwa iwe ni mdima, ndiye kuti mdimawo ni mdima wandiweyani! 24  “Palibe angakhale kapolo wa ambuye aŵili, cifukwa adzadana na mmodzi n’kukonda winayo. Kapena adzakhulupilika kwa mmodzi n’kunyoza winayo. Simungakhale kapolo wa Mulungu komanso wa Cuma pa nthawi imodzi. 25  “Pa cifukwa cimeneci nikukuuzani kuti: Lekani kudela nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya ciyani kapena mudzamwa ciyani, kapenanso za matupi anu kuti mudzavala ciyani. Kodi moyo si wofunika kuposa cakudya, komanso thupi kuposa covala? 26  Yang’anitsitsani mbalame za mumlengalenga. Sizifesa mbewu ayi, kapena kukolola, kapenanso kututila m’nkhokwe. Koma Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa. Kodi inu sindinu ofunika kwambili kuposa mbalame? 27  Ndani wa inu angatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa? 28  Komanso n’cifukwa ciyani mukudela nkhawa za zovala? Phunzilam’poni kanthu pa mmene maluŵa a kuchile amakulila. Sagwila nchito, kapena kupanga nsalu. 29  Koma nikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluŵa amenewa. 30  Lomba ngati umu ni mmene Mulungu amavekela zomela za kuchile, zimene zimangokhalapo lelo, maŵa n’kuziponya pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo a cikhulupililo cocepa inu? 31  Conco musamade nkhawa kuti, ‘Tidzadya ciyani?’ kapena, ‘Tidzamwa ciyani?’ kapenanso kuti, ‘Tidzavala ciyani?’ 32  Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti mukufunikila zinthu zonsezi. 33  “Cotelo pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba na cilungamo cake, ndipo zinthu zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu. 34  Conco musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala na nkhawa zake. Zovuta za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.

Mawu a m'Munsi

Mawu ake enieni, “cilungamo canu.”
Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “lionedwe kuti ni lopatulika; lionedwe kuti ni loyela.”
Mawu ake enieni, “nkhongole zathu.”
Mawu ake enieni, “ali nafe nkhongole.”
Kapena kuti, “mutipulumutse.”
Kapena kuti, “amaleka kudzisamalila.”
Kapena kuti, “limaona bwino.”
Mawu ake enieni, “loipa.”
Mawu ake enieni, “na mkono umodzi.”