Wolembedwa na Mateyo 7:1-29

  • ULALIKI WA PA PHILI (1-27)

    • Lekani kuweluza ena (1-6)

    • Pemphanibe, funa-funanibe, gogodanibe (7-11)

    • Khalidwe Lopambana (12)

    • Geti yopanikiza (13, 14)

    • Mudzawadziŵa na zipatso zawo (15-23)

    • Nyumba yomangidwa pa thanthwe, nyumba yomangidwa pa mcenga (24-27)

  • Khamu la anthu lidabwa na kaphunzitsidwe ka Yesu (28, 29)

7  “Lekani kuweluza ena kuopela kuti inunso mungaweluzidwe;  cifukwa ciweluzo cimene mukuweluza naco ena, inunso mudzaweluzidwa naco, ndipo muyeso umene mukupimila ena, inunso adzakupimilani womwewo.  Nanga n’cifukwa ciyani ukuyang’ana kacitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako?  Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Leka nikucotse kacitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa mtenje wa nyumba?  Wonyenga iwe! Coyamba cotsa mtanda wa nyumba umene uli m’diso lakowo. Ukatelo, udzatha kuona bwino-bwino mmene ungacotsele kacitsotso m’diso la m’bale wako.  “Musamapatse agalu zinthu zopatulika kapena kuponyela nkhumba ngale zanu, kuopela kuti zingaponde-ponde ngalezo na kutembenuka n’kukukhadzulani.  “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; pitilizani kufuna-funa, ndipo mudzapeza; gogodanibe ndipo adzakutsegulilani;  pakuti aliyense wopempha amalandila, ndipo aliyense wofuna-funa amapeza, ndiponso aliyense wogogoda adzamutsegulila.  Ndani wa inu amene mwana wake akamupempha mkate, angamupatse mwala? 10  Kapena akamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11  Cotelo ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wanu wa kumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka zinthu zabwino kwa amene amamupempha! 12  “Conco, zinthu zonse zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo. Ndipo izi n’zimene Cilamulo na zolemba za aneneli zimaphunzitsa. 13  “Loŵani pa geti yopanikiza, cifukwa msewu wotakasuka ukupita ku ciwonongeko, ndipo geti yake ni yaikulu, komanso anthu ambili akuyenda mmenemo; 14  koma geti yoloŵela ku moyo ni yopanikiza, ndiponso msewu wake ni wopanikiza, komanso amene akuyendamo ni ocepa. 15  “Samalani na aneneli onyenga amene amabwela kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ni mimbulu yolusa. 16  Mudzawazindikila na zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa mu mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa citsamba ca minga, amatelo kodi? 17  Mofananamo, mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse woipa umabala zipatso zoipa. 18  Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, ndipo mtengo woipa sungabale zipatso zabwino. 19  Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula n’kuuponya pa moto. 20  Cotelo, anthu amenewo mudzawazindikila mwa zipatso zawo. 21  “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba ayi, koma yekhayo wocita cifunilo ca Atate wanga amene ali kumwamba. 22  Pa tsikulo, ambili adzati kwa ine: ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenele m’dzina lanu, kutulutsa ziŵanda m’dzina lanu, na kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ 23  Koma ine nidzawauza kuti: ‘Sinikudziŵani m’pang’ono pomwe! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu!’ 24  “Conco, aliyense womva mawu anga na kuwacita, adzakhala ngati munthu wanzelu amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25  Ndiyeno kunagwa cimvula camphamvu ndipo madzi anasefukila. Kenako kunabwela cimphepo ndipo cinawomba nyumbayo mwamphamvu, koma sinagwe cifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26  Komanso, aliyense womva mawu angawa koma osawacita, adzakhala ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mcenga. 27  Ndiyeno kunagwa cimvula camphamvu, ndipo madzi anasefukila. Kenako kunabwela cimphepo cimene cinawomba nyumbayo mwamphamvu, ndipo inagwa na kuwonongeka kothelatu.” 28  Yesu atatsiliza kukamba mawu amenewa, khamu la anthulo linadabwa kwambili na kaphunzitsidwe kake, 29  cifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamulilo, osati monga alembi.

Mawu a m'Munsi