Wolembedwa na Mateyo 9:1-38
9 Conco Yesu anakwela bwato n’kuwolokela ku tsidya lina, ndipo analoŵa mu mzinda wakwawo.
2 Kumeneko, anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo ali gone pa macila. Ataona cikhulupililo cawo, Yesu anauza wofa ziwaloyo kuti: “Limba mtima mwanawe, macimo ako akhululukidwa.”
3 Tsopano alembi ena mumtima anati: “Munthu uyu akunyoza Mulungu.”
4 Podziŵa maganizo awo, Yesu anati, “N’cifukwa ciyani mukuganiza zinthu zoipa m’mitima mwanu?
5 Mwa citsanzo, cosavuta n’citi, kukamba kuti, ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka uyambe kuyenda’?
6 Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa munthu ali na mphamvu zokhululukila macimo pa dziko lapansi . . .” kenako anauza wofa ziwaloyo kuti, “Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.”
7 Iye ananyamuka n’kumapita kwawo.
8 Khamu la anthulo litaona zimenezi linagwidwa na mantha, ndipo linatamanda Mulungu amene anapeleka mphamvu zotelo kwa anthu.
9 Atacoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina dzina lake Mateyo, atakhala pansi mu ofesi yokhometsela misonkho, ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” Nthawi yomweyo iye ananyamuka na kumutsatila.
10 Patapita nthawi, Yesu anali kudya m’nyumba, ndipo okhometsa misonkho ambili komanso ocimwa, anabwela n’kuyamba kudya naye pamodzi na ophunzila ake.
11 Koma Afarisi ataona zimenezi anafunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciyani mphunzitsi wanu amadya na okhometsa misonkho komanso ocimwa?”
12 Yesu atamva zimenezi anati: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufuna.
13 Cotelo, pitani mukamvetsetse tanthauzo la mawu akuti: ‘Nifuna cifundo osati nsembe.’ Pakuti n’nabwela kudzaitana anthu ocimwa osati olungama.”
14 Kenako ophunzila a Yohane anabwela kwa iye n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ife na Afarisi timasala kudya, koma ophunzila anu sasala kudya?”
15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati sakhala acisoni ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, amatelo kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pawo, ndipo panthawiyo adzasala kudya.
16 Palibe munthu amene amasokelela cigamba ca nsalu yatsopano pa covala cakunja cakale, cifukwa akatelo cigamba catsopanoco cimaguza covalaco, ndipo pong’ambikapo pamakula kwambili.
17 Ndiponso anthu sathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo, matumba a vinyowo amaphulika, ndipo vinyoyo amatayika matumbawo n’kuwonongeka. Koma anthu amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba atsopano, ndipo zonse ziŵili zimasungika bwino.”
18 Pamene iye anali kuwauza zimenezi, kunafika wolamulila wina amene anamugwadila na kumuuza kuti: “Pano nikukamba, mwana wanga wamkazi ayenela kuti wamwalila. Koma tiyeni mukaike dzanja lanu pa iye, ndipo akhalanso na moyo.”
19 Pamenepo Yesu ananyamuka pamodzi na ophunzila ake n’kumutsatila.
20 Tsopano mayi wina wodwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, anamuyandikila kumbuyo kwake n’kugwila ulusi wopota wa covala cake cakunja,
21 cifukwa mumtima mwake anali kunena kuti: “Nikangogwila covala cake cakunja, nicila ndithu.”
22 Pamenepo Yesu anatembenuka, ndipo atamuona anati: “Limba mtima mwanawe! Cikhulupililo cako cakucilitsa.” Kucokela ola limenelo, mayiyo anacila.
23 Ndiyeno Yesu ataloŵa m’nyumba ya wolamulila uja, anaona anthu oliza zitolilo, komanso anthu ambili akulila mokweza.
24 Ndiyeno Yesu anati: “Tulukani, cifukwa mtsikana wamng’onoyu sanamwalile koma wagona.” Anthuwo atamva zimenezi anayamba kumuseka monyodola.
25 Atangowatulutsa panja anthuwo, Yesu analoŵa n’kugwila dzanja la mtsikanayo, ndipo iye anauka.
26 Nkhani imeneyi inafala m’dela lonselo.
27 Yesu pocoka kumeneko, amuna aŵili akhungu anam’tsatila. Iwo anali kufuula, amvekele: “Ticitileni cifundo inu Mwana wa Davide.”
28 Ataloŵa m’nyumba, akhungu aja anafika kwa Yesu, ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi muli na cikhulupililo cakuti ningacite zimenezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde Ambuye.”
29 Kenako anawagwila m’maso na kuwauza kuti: “Zicitike mogwilizana na cikhulupililo canu.”
30 Pamenepo anayamba kuona. Ndiyeno Yesu anawacenjeza mwamphamvu kuti: “Samalani kuti aliyense asadziŵe zimenezi.”
31 Koma atatuluka panja, anafalitsa za iye m’dela lonselo.
32 Pamene iwo anali kucoka, anthu anamubweletsela munthu wosalankhula wogwidwa na ciŵanda.
33 Ciŵandaco atacitulutsa, munthu wosalankhulayo anayamba kulankhula. Khamu la anthulo litaona zimenezi, linadabwa kwambili ndipo linati: “Zotelezi sitinazionepo mu Isiraeli.”
34 Koma Afarisi anali kunena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziŵanda na mphamvu za wolamulila ziŵanda.”
35 Ndiyeno Yesu anayamba ulendo woyendela mizinda na midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikila uthenga wabwino, na kucilitsa matenda a mtundu uliwonse komanso zofooka zilizonse.
36 Ataona cikhamu ca anthuwo, anawamvela cisoni cifukwa anali omyuka-myuka komanso otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.
37 Kenako iye anauza ophunzila ake kuti: “Zoonadi, zokolola n’zoculuka, koma anchito ni ocepa.
38 Conco pemphani mwini zokolola kuti atumize anchito okakolola.”