Wolembedwa na Maliko 13:1-37

  • CIMALIZILO CA NTHAWI INO (1-37)

    • Nkhondo, zivomezi, njala (8)

    • Uthenga wabwino udzalalikidwa (10)

    • Cisautso cacikulu (19)

    • Kubwela kwa Mwana wa munthu (26)

    • Fanizo la mtengo wa mkuyu (28-31)

    • Khalanibe maso (32-37)

13  Pamene Yesu anali kutuluka m’kacisi, mmodzi wa ophunzila ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, onani kukongola kwa miyalayi na nyumbazi!”  Koma Yesu anamufunsa kuti: “Kodi waziona nyumba zikulu-zikulu zokongolazi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”  Atakhala pansi m’Phili la Maolivi, moyang’ana kumene kunali kacisi, Petulo, Yakobo, Yohane, na Andireya anamufunsa mwamseli kuti:  “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti? Nanga cizindikilo cakuti zinthu zonsezi zili pafupi kufika kumapeto cidzakhala ciyani?”  Conco, Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusoceletseni.  Ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasoceletsa anthu ambili.  Ndiponso mukadzamva phokoso la nkhondo komanso mbili za nkhondo, musadzacite mantha. Zimenezi ziyenela kucitika, koma mapeto adzakhala asanafikebe.  “Mtundu udzaukilana na mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana na ufumu wina. Kudzakhala zivomezi m’malo osiyana-siyana, komanso kudzakhala njala. Zinthu zonsezi ni ciyambi ca masautso.*  “Koma inu samalani. Anthu adzakupelekani ku makhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge na kukupelekani kwa abwanamkubwa na mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo. 10  Komanso uthenga wabwino uyenela kulalikidwa ku mitundu yonse coyamba. 11  Ndipo akakutengani kuti akakupelekeni, musade nkhawa kuti mukakamba ciyani. Koma mukakambe zilizonse zimene mudzapatsidwa nthawi yomweyo, pakuti amene adzakamba si inuyo ayi, koma mzimu woyela. 12  Komanso munthu adzapeleka m’bale wake kuti aphedwe, tate adzapeleka mwana wake, ndipo ana adzaukila makolo awo n’kuwapeleka kuti aphedwe. 13  Anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. Koma amene adzapilile* mpaka pa mapeto adzapulumuka. 14  “Koma mukadzaona cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko citaimilila pa malo amene siciyenela kuima (woŵelenga adzazindikile), pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila ku mapili. 15  Munthu amene adzakhale pa mtenje asadzatsike kapena kuloŵa m’nyumba mwake kuti akatenge cinthu ciliconse. 16  Ndipo munthu amene adzakhale ku munda, asadzabwelele ku zinthu zimene wasiya kumbuyo kuti akatenge covala cake cakunja. 17  Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! 18  Pitilizani kupemphela kuti zimenezi zisadzacitike m’nyengo yozizila, 19  cifukwa masiku amenewo kudzakhala cisautso cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu analenga mpaka pa nthawiyo, ndipo sicidzacitikanso. 20  Kukamba zoona, Yehova akanapanda kucepetsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwa amene iye wawasankha, adzacepetsa masikuwo. 21  “Komanso munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena kuti, ‘Onani! Ali uko,’ musakakhulupilile. 22  Pakuti kudzabwela anthu onamizila kukhala Khristu komanso aneneli onyenga, ndipo adzacita zizindikilo na zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, asoceletse osankhidwawo. 23  Conco samalani. Ine nakuuzilantoni zinthu zonse. 24  “Koma m’masiku amenewo cisautsoco cikadzatha, dzuŵa lidzacita mdima, ndipo mwezi sudzawala. 25  Komanso nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba, ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka. 26  Ndiyeno iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela m’mitambo, ali na mphamvu zazikulu komanso ulemelelo. 27  Kenako iye adzatumiza angelo ake ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinayi, kucokela ku malekezelo a dziko mpaka ku malekezelo a kumwamba. 28  “Tsopano phunzilamponi kanthu pa fanizo ili la mtengo wa mkuyu. Mukangoona kuti nthambi yake yanthete yayamba kuphuka na kutulutsa masamba, mumadziŵa kuti dzinja layandikila. 29  Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zimenezi zikucitika, mukadziŵe kuti iye ali pafupi, pa khomo penipeni. 30  Ndithu nikukuuzani, m’badwo uwu sudzatha wonse mpaka zinthu zonsezi zitacitika. 31  Kumwamba na dziko lapansi zidzacoka, koma mawu anga sadzacoka ayi. 32  “Ponena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene adziŵa, ngakhale angelo kumwamba kapena Mwanayo, koma Atate yekha basi. 33  Khalani maso, khalani chelu, cifukwa nthawi yoikika simukuidziŵa. 34  Zili monga munthu amene anasiya nyumba yake n’kupita ku dziko lina, ndipo anapatsa akapolo ake ulamulilo. Aliyense anamupatsa nchito yake, komanso analamula mlonda wa pakhomo kuti akhalebe maso. 35  Conco khalanibe maso cifukwa simukudziŵa nthawi imene mwininyumba adzabwela, kaya ni madzulo, pakati pa usiku, m’matandakuca* kapena m’mamaŵa, 36  kuti iye akadzabwela modzidzimutsa, asadzakupezeni mutagona. 37  Koma zimene nikukuuzani nikuuza onse kuti: Khalanibe maso.”

Mawu a m'Munsi

Mawu ake enieni, “zoŵaŵa za pobeleka.”
Kapena kuti, “amene wapilila.”
Mawu ake eni-eni, “tambala akulila.”