UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO April 2016

Maulaliki Acitsanzo

Maulaliki acitsanzo ogaŵila Galamukani! ndi buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa. Seŵenzetsani maulaliki acitsanzo amenewa kuti mukonze ulaliki wanu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Limbikitsani Ena ndi Mau Abwino

Anzake atatu a Yobu sanamutonthoze, koma anangoonjezela mavuto ake mwa kukamba mau oipa ndi kumuimba mlandu. (Yobu 16-20)

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Mbali Yatsopano Yoyambitsila Makambilano

Yambani kukambilana nkhani za m’Baibulo poseŵenzetsa mbali yatsopano yakuti “Kodi Baibulo Limakamba Ciani?”

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Yobu Anapewa Maganizo Olakwika

Onani kusiyana pakati pa mabodza a Satana ndi mmene Yehova amationela. (Yobu 21-27)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Yobu Anali Citsanzo Cabwino Pankhani Yosunga Umphumphu

Yobu anali wokonzeka kutsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino, ndi kutengela cilungamo ca Mulungu. (Yobu 28-32)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Bwenzi Lenileni Limapeleka Uphungu Wolimbikitsa

Tengelani mmene Elihu anacitila zinthu mwacikondi kwa mnzake Yobu. (Yobu 33-37)

KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI

Nchito Yogaŵila Tumapepala Toitanila Anthu ku Msonkhano Wacigawo

Zimene mufunika kudziŵa pamene muitanila anthu ku msonkhano wacigawo wa Mboni za Yehova. Yesezani maulaliki acitsanzo.

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Zikumbutso za Msonkhano Wacigawo

Ganizilani mmene mungaonetsele ena cikondi pa msonkhano wacigawo.