Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 21-27

Yobu Anapewa Maganizo Olakwika

Yobu Anapewa Maganizo Olakwika

Satana amaseŵenzetsa mabodza pofuna kufooketsa atumiki a Yehova masiku ano. Onani mmene mabodza a Satana amasiyanilana ndi mmene Yehova amaonela zinthu, malinga ndi mmene buku la Yobu likuonetsela. Lembani mndandanda wa Malemba ena oonjezela amene angakuthandizeni kuona kuti Yehova amakusamalilani.

MABODZA A SATANA

MMENE YEHOVA AMAONELA ZINTHU

Mulungu ndi wovuta kwambili kumusangalatsa, cakuti palibe ciliconse cimene atumiki ake amacita cimene iye amasangalala naco. Ngakhale cilengedwe sicimukondweletsa. (Yobu 4:18; 25:5)

Yehova amayamikila kudzipeleka kwathu (Yobu 36:5)

Munthu ndi wacabecabe kwa Mulungu (Yobu 22:2)

Yehova amavomeleza ndi kudalitsa utumiki wathu umene timacita mokhulupilika (Yobu 33:26; 36:11)

Mulungu alibe nazo nchito zakuti mukucita zinthu mwacilungamo (Yobu 22:3)

Yehova amayang’anila anthu olungama ndi okhulupilika (Yobu 36:7)