Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI

Nchito Yogaŵila Tumapepala Toitanila Anthu ku Msonkhano Wacigawo

Nchito Yogaŵila Tumapepala Toitanila Anthu ku Msonkhano Wacigawo

Caka ciliconse, timayembekezela kucita phwando la kuuzimu pa misonkhano yathu yacigawo. Conco, tiyenela kuitana anthu mmene tingathele kuti adzacite nafe msonkhanowu, kuti naonso akaone kuti Yehova ndi wabwino. (Sal. 34:8) Bungwe lililonse la akulu lidzapanga makonzedwe a mmene tingagaŵile tumapepala twa ciitano tumenetu.

ZIMENE MUFUNIKA KUDZIŴA

  • Kodi msonkhano wacigawo udzacitika liti?

  • Kodi mpingo udzayamba liti kugaŵila tumapepala twa ciitano?

  • Ndi liti pamene mpingo umakumana kuti ukonzekele kupita mu ulaliki?

  • Kodi ndaika zolinga zotani ponena za kugaŵila tumapepala twa ciitano?

  • Kodi ndidzaitana ndani?

KODI MUDZAKAMBA CIANI?

Mukapatsana moni, mungakambe kuti:

“Tikugwila nchito yapadela imene ikucitika padziko lonse yoitanila anthu ku cocitika cofunika kwambili. Deti, nthawi, ndi malo zalembedwa pa kapepala aka ka ciitano. Tidzasangalala kuona kuti mwapezekapo.”

MMENE MUNGAKULITSILE CIDWI

Ngakhale kuti tifuna kuitanila anthu ambili ku msonkhano wacigawo, tifunika kukhala chelu kuti tithandize anthu amene aonetsa cidwi.

Kumapeto kwa mlungu, mungagaŵile magazini pamodzi ndi kapepala ka ciitano.