Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 33-37

Bwenzi Lenileni Limapeleka Uphungu Wolimbikitsa

Bwenzi Lenileni Limapeleka Uphungu Wolimbikitsa

Elihu atayamba kukamba, uphungu umene anapeleka unali wosiyana kwambili ndi wa Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari, ponse paŵili m’mau ake ndi mmene anacitila ndi Yobu. Iye anaonetselatu kuti anali bwenzi lenileni komanso mlangizi wabwino, wofunika kutsatila citsanzo cake.

MAKHALIDWE AMENE MLANGIZI WABWINO AMAKHALA NAO

ELIHU ANATISIILA CITSANZO CABWINO

32:4-7, 11, 12; 33:1

 

  • KULEZA MTIMA

  • KUMVETSELA

  • ULEMU

 
  • Moleza mtima, Elihu anayembekeza amuna acikulile kuti atsilize kukamba, pambuyo pake iye anayamba kukamba

  • Kumvetsela mosamala, kunamuthandiza kumvetsetsa nkhani yonse asanapeleke uphungu

  • Iye anali kuchula dzina la Yobu pokamba naye ndipo analankhula monga bwenzi lake

 

33:6, 7, 32

 

  • KUDZICEPETSA

  • KUFIKILIKA

  • CIFUNDO

 
  • Elihu anali wodzicepetsa ndi wokoma mtima, ndipo anavomeleza kuti anali wopanda ungwilo

  • Anacitila cifundo Yobu pamene anali kuvutika

 

33:24, 25; 35:2, 5

 

  • KUCITA ZINTHU MOYENELELA

  • KUKOMA MTIMA

  • KUPHUNZITSIDWA NDI MULUNGU

 
  • Mokoma mtima, Elihu anathandiza Yobu kuzindikila kuti maganizo ake anali olakwika

  • Elihu anathandiza Yobu kuona kuti kudziona kuti ndi wolungama sicinali cinthu cofunika kwambili

  • Uphungu womveka bwino wa Elihu unathandiza Yobu kukhala wokonzeka kulandila malangizo ocokela kwa Yehova