Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Zikumbutso za Msonkhano Wacigawo

Zikumbutso za Msonkhano Wacigawo

Nthawi zonse timafuna kuonetsa kuti timakonda Mulungu ndi anzathu pa nthawi ya msonkhano wacigawo. (Mat. 22:37-39) Lemba la 1 Akorinto 13:4-8 limati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi . . . sicicita zosayenela, sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya. . . . Cikondi sicitha.” Conco, pamene muonelela vidiyo ya Zikumbutso za Msonkhano Wacigawo, ganizilani njila zimene mungaonetsele cikondi kwa ena pa msonkhano wacigawo.

KODI TINGAONETSE BWANJI CIKONDI . . .

  • posungila ena malo okhala?

  • nyimbo za malimba zikayamba?

  • pamalo ogona m’dela limene mukucitikila msonkhano?

  • pogwila nchito yodzifunila?