Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Mbali Yatsopano Yoyambitsila Makambilano

Mbali Yatsopano Yoyambitsila Makambilano

Kuyambila ndi Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya Na. 1 2016, patsamba lothela pakhala pakupezeka mbali yakuti “Kodi Baibulo Limakamba Ciani?” Mbali yatsopano imeneyi yakonzedwa kuti itithandize kuyamba kukambilana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Mbaliyi yakonzedwa mofanana ndi tumapepala twauthenga. Pali funso ndi yankho la m’Malemba, komanso mfundo zina zofunika kukambilana.

Makambilano osangalatsa ozikidwa pa nkhani za m’malemba, amatithandiza kuyambitsa maphunzilo a Baibulo. Seŵenzetsani mbali imeneyi pothandiza anthu kuthetsa njala yao ya kuuzimu.—Mat. 5:6.

MMENE TINGASEŴENZETSELE MBALI IMENEYI:

  1. Funsani mwininyumba funso limodzi pa mafunso amene alipo

  2. Mvetselani mosamala ndipo muyamikileni pa yankho lake

  3. Ŵelengani lemba limene lili pa kamutu kakuti, “Zimene Baibulo Limakamba,” ndipo m’funseni maganizo ake pa vesi limenelo. Ngati ali ndi nthawi, pitilizani kukambilana mfundo imene ili pa kamutu kakuti “Zina Zimene Baibulo Limakamba.”

  4. Gaŵilani magazini

  5. Pangani makonzedwe akuti mukabweleleko kudzakambilana funso laciŵili