UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mukhoza Kulimbikitsa Mkhristu Wozilala
Pa ciŵili, April 11, Akhristu ozilala ambili adzapezeka pa Cikumbutso. Anayamba bwino kuthamanga pa mpikisano wa moyo, koma afooka pa zifukwa zosiyana-siyana. Zifukwa zina azifotokoza m’kabuku kakuti Bwelelani kwa Yehova. (Aheb. 12:1) Ngakhale n’conco, ozilala amenewa ni amtengo wapatali kwa Yehova cifukwa anawagula na magazi a Mwana wake. (Mac. 20:28; 1 Pet. 1:18, 19) Nanga tingawathandize bwanji kuti abwelele ku mpingo?
Akulu a mpingo amasakila anthu ozilala kuti awathandize, monga mmene m’busa amasakilila mwakhama nkhosa zimene zasocela. (Luka 15:4-7) Izi zimaonetsa cikondi na cisamalilo ca Yehova. (Yer. 23:3, 4) Koma si akulu okha, tonse tikhoza kuwalimbikitsa ozilala. Khama lathu poonetsa kukoma mtima na cikondi zimam’kondweletsa Yehova, ndipo zingabweletse mapindu osaneneka. (Miy. 19:17; Mac. 20:35) Conco, ganizilani amene mungam’limbikitse, ndipo teloni mwamsanga.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI LIMBIKITSANI OZILALA, NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
-
N’ciani cimene Abbey anacita atakumana ndi wa Mboni amene sanali kudziŵana naye?
-
N’cifukwa ciani tiyenela kudziŵitsa akulu ngati taganiza zothandiza munthu wozilala?
-
Kodi Abbey anakonzekela bwanji pokacezela Laura kaciŵili?
-
Kodi Abbey anaonetsa bwanji khama, kuleza mtima, na cikondi poyetsa kulimbikitsa Laura?
-
Tingaphunzilenji pa fanizo la Yesu la pa Luka 15:8-10?
-
Ni madalitso anji amene anatsatilapo cifukwa ca khama la Akhristu osiyana-siyana pothandiza Laura?