April 17- 23
YEREMIYA 25-28
Nyimbo 137 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khalani Wolimba Mtima Monga Yeremiya”: (10 min.)
Yer. 26:2-6—Yehova anauza Yeremiya kulengeza uthenga wa cenjezo (w09 12/1 peji 24 pala. 6)
Yer. 26:8, 9, 12, 13—Yeremiya sanayope adani ake pomuopseza (jr peji 21 pala. 13)
Yer. 26:16, 24—Yehova anateteza mneneli wake wolimba mtimawo (w09 12/1 peji 25 pala. 1)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 27:2, 3—N’cifukwa ciani amithenga ocokela ku mitundu yosiyana-siyana anabwela ku Yerusalemu? Ndipo n’cifukwa ciani Yeremiya anawapangila magoli? (jr peji 27 pala. 21)
Yer. 28:11—Kodi Yeremiya anaonetsa bwanji kuzindikila pamene Hananiya anam’tsutsa? Nanga tingaphunzilepo ciani? (jr peji 187-188 mapa. 11-12)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 27:12-22
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) T-36—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) T-36—Yalani maziko a ulendo wobwelelako wotsatila.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) lv peji 7 mapala. 4-5—Onetsani mmene mungafikile pamtima wophunzila.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Nyimbo Imene Inalimbikitsa Akaidi (yendani kumavidiyo ZOCITIKA NA KUFUNSA MAFUNSO).
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 11 mapala. 9-21
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 26 na Pemphelo