Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 25-28

Khalani Wolimba Mtima Monga Yeremiya

Khalani Wolimba Mtima Monga Yeremiya

Yeremiya anacenjeza kuti Yerusalemu adzasakazidwa mofanana ndi mzinda wa Silo

26:6

  • Pa nthawi ina likasa la pangano, loimila Yehova, linali kusungidwila ku Silo

  • Yehova analola kuti Afilisiti alande likasalo, ndipo siinabwelelenso ku Silo

Ansembe, aneneli, ndi anthu onse anaopseza kuti adzamupha Yeremiya

26:8, 9, 12, 13

  • Anthu anam’gwila Yeremiya cifukwa colosela zakuti kacisi adzawonongedwa

  • Yeremiya sanaope ndi kuthaŵa

Yehova anam’teteza Yeremiya

26:16, 24

  • Yeremiya anakhalabe wolimba mtima, ndipo Yehova sanamusiye

  • Mulungu anacititsa Ahikamu wolimba mtima kuteteza Yeremiya

Yeremiya sanaleke kulengeza uthenga umene anthu anali kukwiya nawo cifukwa Yehova anali kumucilikiza na kumulimbikitsa kwa zaka 40