Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima

Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima

Pamene Paulo na Sila anali m’ndende, anatamanda Mulungu ndi nyimbo. (Mac. 16:25) M’zaka zamakono, okhulupilila anzathu anali kuimba nyimbo za Ufumu m’ndende ya Sachsenhausen pa nthawi ya cipani ca Nazi ku Germany, ndiponso pamene anali m’ndende ku Siberia. Zitsanzozi zionetsa kuti nyimbo zimathandiza Akhristu kukhala olimba mtima panthawi ya mayeselo.

Posacedwa, tidzalandila buku la nyimbo zatsopano lakuti “Imbani mwa Cisangalalo” kwa Yehova. Tikadzalandila buku limeneli, tidzakhomeleze mau ake pamtima mwa kumaimba nyimbozo pa kulambila kwa pabanja. (Aef. 5:19) Tikatelo, mzimu woyela udzatithandiza kuzikumbukila nyimbozo panthawi ya mayeselo. Nyimbo za Ufumu zimatithandiza kusumika maganizo pa ciyembekezo cathu. Zimalimbikitsa ngako pamayeselo. Cina, pamene tili acimwemwe, mau otsitsimula a nyimbo amatithandiza ‘kuimba mwacisangalalo,’ cifukwa comvela bwino mumtima. (1 Mbiri 15:16; Sal. 33:1-3) Tiyeni tonse tikapindule nazo mokwanila nyimbo zathu za Ufumuzo.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI NYIMBO IMENE INALIMBIKITSA AKAIDI. NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’ciani cinacititsa M’bale Frost kupeka nyimbo?

  • Kodi nyimbo zinawathandiza bwanji abale m’ndende ya Sachsenhausen?

  • Ni pa zocitika za tsiku na tsiku ziti pamene nyimbo za Ufumu zingakulimbikitseni?

  • Ni nyimbo za Ufumu ziti zimene mungakonde kuziika pamtima?