April 3- 9
YEREMIYA 17-21
Nyimbo 69 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Lolani Kuti Yehova Aumbe Maganizo na Khalidwe Lanu” (10 min.)
Yer. 18:1-4—Woumba amakhala na ulamulilo pa dothi lake (w99 4/1 peji 22 pala. 3)
Yer. 18:5-10—Yehova ali na ulamulilo pa anthu (it-2 peji 776 pala. 4)
Yer. 18:11—Lolani kuti Yehova akuumbeni (w99 4/1 peji 22 mapala. 4-5)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 17:9—Kodi cinyengo ca mtima cingaonekele bwanji? (w01 10/15 peji 25 pala. 13)
Yer. 20:7—Kodi Yehova anaseŵenzetsa bwanji mphamvu zake pa Yeremiya na kum’putsitsa? (w07 3/15 peji 9 pala. 6)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 21:3-14
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani vidiyo yake iliyonse, ndiyeno kambilanani zimene mwaphunzilapo. Limbikitsani onse kupanga maulendo obwelelako kwa anthu amene analandila kapepa kauthenga kakuti Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zosoŵa za Pampingo: (5 min.) Apo ayi, kambilanani zimene mwaphunzilapo mu Buku Lapacaka. (yb16 22)
“Alandileni Bwino”: (10 min.) Yambani ndi nkhani ya 3 mineti. Tsilizani mwa kutambitsa vidiyo yakuti Steve Gerdes: Sitidzaiŵala Moni Umene Anatipatsa (yendani ku mavidiyo ZOCITIKA NA KUFUNSA MAFUNSO).
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 10 mapala. 12-19, bokosi pa peji 105 (kulamanja), na bokosi lobwelelamo pa peji 107
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 5 na Pemphelo