Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WACIKHRISTU

Alandileni Bwino

Alandileni Bwino

Kulandila ndani? Aliyense wobwela kumisonkhano yathu—kuyambila okondwelela atsopano mpaka mabwenzi athu anthawi zonse. (Aroma 15:7; Aheb. 13:2) Akhoza kukhala mboni inzathu yocokela ku dziko lina, kapena wozilala amene wabwela kumisonkhano pambuyo pa zaka. Ganizilani ngati munali imwe. Kodi simunakamva bwino kukulandilani ndi moni wotentha? (Mat. 7:12) Conco, bwanji osakhalako na cizolowezi cozungulila mu Nyumba ya Ufumu, kupatsa moni uyu na uyu misonkhano isanayambe na pambuyo pake? Izi zimapangitsa malo a msonkhano kukhala okondweletsa ndi aubwenzi, ndipo Yehova amalemekezeka. (Mat. 5:16) N’zoona kuti sizingatheke kukamba na munthu aliyense. Koma ngati tonse ticitako zimenezi, aliyense adzamva kuti walandilidwa. *

Mzimu weni-weni woceleza tiyenela kuuonetsa nthawi zonse, osati cabe pa zocitika zapadela monga pa Cikumbutso. Alendo akaona cikondi cacikhristu cimene tiwaonetsa, angayambe kutamanda Mulungu ndi kugwilizana nafe pa kulambila koyela.—Yoh. 13:35.

^ par. 3 Motsatila mfundo za m’Baibo, tifunika kupewa kuyanjana ndi ocotsedwa kapena ozilekanitsa amene angabwele ku misonkhano.—1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10.