UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO April 2018
Makambilano Acitsanzo
Makambilano otsatizana-tsatizana okamba za Baibo na banja lacimwemwe.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Pasika na Cikumbutso—Kulingana na Kusiyana Kwake
Ngakhale kuti Pasika siinali kucitila cithunzi Cikumbutso ca imfa ya Yesu Khristu, zinthu zina za pa Pasika zili na tanthauzo kwa ise.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Pitani Mukapange Ophunzila—Cifukwa ciani, Kuti, ndipo Motani?
Kupanga ophunzila kumatanthauza kuphunzitsa anthu zinthu zonse zimene Yesu anatilamula. Nchito yathu yopanga ophunzila imaphatikizapo kuthandiza ophunzila kuseŵenzetsa zimene Yesu anatilamula na kutengela citsanzo cake.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kulalikila na Kuphunzitsa—N’kofunika pa Nchito Yopanga Ophunzila
Yesu analamula otsatila ake kukapanga ophunzila. Kodi nchitoyi imaphatikizapo ciani? Kodi tingawathandize bwanji anthu kupita patsogolo mwauzimu?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Macimo Ako Akhululukidwa”
Tiphunzilapo ciani pa cozizwitsa copezeka pa Maliko 2:5-12? Kodi cocitika ici cingatithandize bwanji kupilila tikadwala?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kucilitsa pa Sabata
N’cifukwa ciani Yesu anamva cisoni kwambili na zocita za atsogoleli a cipembedzo aciyuda? Ni mafunso ati amene tingadzifunse kuti tione ngati tikutengela cifundo ca Yesu?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Yesu Ali na Mphamvu Zokaukitsa Okondedwa Athu Amene Anamwalila
Kusinkha-sinkha nkhani za m’Baibo zokhudza ciukililo kudzalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti m’tsogolo akufa adzauka.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kuseŵenzetsa Mwaluso Zida Zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu
Kuti tiphunzitse mogwila mtima, tifunika kudziŵa moseŵenzetsela zida zathu. Kodi cida cathu cacikulu n’ciani? Tinganole bwanji luso lathu loseŵenzetsa zida zophunzitsila za mu Thuboksi yathu?