April 23-29
MALIKO 3-4
Nyimbo 77 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kucilitsa pa Sabata”: (10 min.)
Maliko 3:1, 2—Atsogoleli a cipembedzo aciyuda anali kufuna-funa pom’pezela cifukwa Yesu (jy peji 78 mapa. 1-2)
Maliko 3:3, 4—Yesu anadziŵa kuti anthuwo anali na maganizo olakwika kwambili osacokela m’malemba pa za lamulo la Sabata. (jy peji 78 pala. 3)
Maliko 3:5—Yesu anamva “cisoni kwambili cifukwa ca kuuma mtima kwawo.” (“mokwiya ndi kumva cisoni kwambili” nwtsty mfundo younikila)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Maliko 3:29—Kodi kunyoza mzimu woyela kumatanthauza ciani? Nanga kumabweletsa mavuto anji? (“wanyoza mzimu woyela,” “mlandu wa chimo losatha” nwtsty mfundo younikila)
Maliko 4:26-29—Kodi tingaphunzilepo ciani pa fanizo la Yesu la wofesa mbeu amene amagona? (w14 12/15 mape. 12-13 mapa. 6-8)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Maliko 3:1-19a
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kubwelelako Kaciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo.
Kubwelelako Kacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Sankhani mwekha lemba na kugaŵila cofalitsa cophunzitsila Baibo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs peji 36 mapa. 21-22—Onetsani mmene mungamufikile pamtima.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Amene Ali ndi Makutu Akumva, Amve.”: (15 min.) Fotokozani zimene Maliko 4:9 itanthauza (nwtsty mfundo younikila). Tambitsani vidiyo yakuti Khalani Anzelu mwa Kulandila Uphungu. Ndiyeno, kambilanani zocokela m’buku la ‘Khalanibe M’cikondi ca Mulungu’ pa mapeji 46-47.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 18
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 123 na Pemphelo