April 30–May 6
MALIKO 5-6
Nyimbo 151 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yesu Ali na Mphamvu Zokaukitsa Okondedwa Athu Amene Anamwalila”: (10 min.)
Maliko 5:38—Timalila ngati munthu amene timakonda wamwalila
Maliko 5:39-41—Yesu ali na mphamvu zokaukitsa anthu amene “akugona” mu imfa (“sanamwalile ayi, koma akugona” nwtsty mfundo younikila pa Maliko 5:39)
Maliko 5:42—Ciukililo cam’tsogolo cidzacititsa anthu ‘kusangalala kwambili’ (jy peji 118 pala. 6)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Maliko 5:19, 20—N’cifukwa ciani malangizo a Yesu panthawiyi anasiyana ndi a nthawi zonse? (“ukawauze” nwtsty mfundo younikila pa Maliko 5:19)
Maliko 6:11—Kodi ‘kusansa fumbi kumapazi’ kutanthauza ciani? (“sansani fumbi kumapazi anu” nwtsty mfundo younikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Maliko 6:1-13
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kubwelelako Kaciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Onetsani mwininyumba webusaiti yathu ya jw.org.
Kubwelelako Kacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Dzisankhileni mwekha lemba, na funso lokakambilana pa ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs mape. 36 pala. 23-24—Onetsani mmene mungamufikile pa mtima.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kuseŵenzetsa Mwaluso Zida Zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu”: (5 min.) Kukambilana.
Kupeza Citonthozo m’Gulu la Yehova: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani mafunso aya: Kodi banja la m’bale Pera linakumana na mavuto anji? N’ciani cinawathandiza kupilila? N’cifukwa ciani tifunika kukhalabe okangalika mwauzimu pamene takumana na mavuto?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 19 mapa. 1-9
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 72 na Pemphelo