UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kuseŵenzetsa Mwaluso Zida Zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu
Kupanga ophunzila kuli ngati kumanga nyumba. Kuti tiimange bwino nyumbayo, tifunika kudziŵa moseŵenzetsela zida zomangila. Tiyenela kukulitsa luso lathu loseŵenzetsa Mau a Mulungu, amene ndico cida cathu cacikulu. (2 Tim. 2:15) Tiyenelanso kuseŵenzetsa mwaluso zofalitsa zina na mavidiyo a mu Thuboksi yathu ya zida Zophunzitsila—tili na colinga copanga ophunzila. *
Munganole bwanji luso lanu loseŵenzetsa zida zophunzitsila za mu Thuboksi yathu? (1) Pemphani woyang’anila kagulu kanu kuti akuthandizeni, (2) lalikilani pamodzi na wofalitsa amene ni ciyambakale kapena mpainiya, ndipo (3) muziyeseza. Ngati museŵenzetsa mwaluso zofalitsa zimenezi na mavidiyo, mudzakhala acimwemwe pogwila nchito yomanga yauzimu imene ikucitika pali pano.
MAGAZINI
TUMABUKU
MABUKU
TUMAPEPA TWA UTHENGA
MAVIDIYO
TUMAPEPA TWA CIITANILO
TUMAKADI TONGENELA PA WEBUSAITI
^ par. 3 Zofalitsa zocepa zimene sizipezeka mu Thuboksi yathu anazilembela magulu ena-ake a anthu. Zofalitsazi tingaziseŵenzetse pakakhala pofunikila.