April 1-7
1 AKORINTO 7-9
Nyimbo 136 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Umbeta ni Mphatso”: (10 min.)
1 Akor. 7:32—Akhristu amene ni mbeta angatumikile Yehova popanda nkhawa zimene anthu ali pabanja amakhala nazo (w11 1/15 18 ¶3)
1 Akor. 7:33, 34—Akhristu ali pabanja “amadela nkhawa zinthu za dziko” (w08 7/15 27 ¶1)
1 Akor. 7:37, 38—Akhristu amene amakhalabe mbeta kuti akwanilitse zolinga zawo zauzimu, ‘amacita bwino’ kuposa Akhristu ali pabanja (w96 10/15 12-13 ¶14)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
1 Akor. 7:11—Ni mavuto otani amene angapangitse Mkhristu kuganizila zopatukana na mnzake wa m’cikwati? (lvs 251)
1 Akor. 7:36—N’cifukwa ciani Akhristu afunika kukwatila kapena kukwatiwa kokha ‘ngati apitilila pacimake pa unyamata’? (w00 7/15 31 ¶2)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) 1 Akor. 8:1-13 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kachulidwe ka Malemba Koyenela, ndiyeno kambilanani phunzilo 4 m’bulosha ya Kuphunzitsa.
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w12 11/15 20—Mutu: Kodi Anthu Amene Amasankha Kukhalabe Paumbeta Amalandila Mphatsoyi M’njila Yapadela? (th phunzilo 12)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Cititsani Umbeta Wanu Kukhala Wopambana: (15 min.) Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno, kambilanani mafunso aya: Kodi Akhristu amene ni mbeta amakumana na vuto lanji? (1 Akor. 7:39) N’cifukwa ciani mwana wamkazi wa Yefita ni citsanzo cabwino? Kodi Yehova amawacitila ciani anthu okhulupilika? (Sal. 84:11) Kodi mpingo ungawalimbikitse bwanji anthu amene ni mbeta? Kodi Akhristu amene sali pa banja angaciteko mautumiki ati?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 61
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 42 na Pemphelo