April 6-12
Pa Ciŵili, April 7, 2020—Cikumbutso ca Imfa ya Khristu
Caka ciliconse pa nyengo ya Cikumbutso, Akhristu ambili amasinkha-sinkha pa cikondi cacikulu cimene Yehova Mulungu na Mwana wake Yesu Khristu anationetsa. (Yoh. 3:16; 15:13) Mungaseŵenzetse chati ili pansipa kuti mupeze malemba m’Mauthenga Abwino amene amafotokoza zimene Yesu anacita ku Yerusalemu asanaphedwe. Zocitika zimenezi zifotokozedwa bwino m’cigawo 6 ca buku lakuti Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo. Kodi cikondi ca Mulungu na Khristu cikulimbikitsani kucita ciani?—2 Akor. 5:14, 15; 1 Yoh. 4:16, 19.
UTUMIKI WOMALIZA WA YESU MU YERUSALEMU
Nthawi |
Malo |
Cocitika |
Mateyu |
Maliko |
Luka |
Yohane |
---|---|---|---|---|---|---|
33, Nisani 8 (April 1-2, 2020) |
Betaniya |
Yesu afika masiku 6 Pasika asanayambe |
|
|
|
11:55–12:1 |
Nisani 9 (April 2-3, 2020) |
Betaniya |
Mariya athila mafuta m’mutu mwa Yesu na kumapazi kwake |
|
12:2-11 |
||
Betaniya- Betefage- Yerusalemu |
Aloŵa mu Yerusalemu mwacisangalalo, atakwela pa bulu |
19:29-44 |
12:12-19 |
|||
Nisani 10 (April 3-4, 2020) |
Betaniya- Yerusalemu |
Atembelela mtengo wa mkuyu; ayeletsanso kacisi |
19:45, 46 |
|
||
Yerusalemu |
Mkulu wansembe ndi alembi akonza ciwembu cofuna kupha Yesu |
|
19:47, 48 |
|
||
Yehova alankhula; Yesu anenelatu za imfa yake; kusakhulupilila kwa Ayuda kukwanilitsa ulosi wa Yesaya |
|
|
|
12:20-50 |
||
Nisani 11 (April 4-5, 2020) |
Betaniya- Yerusalemu |
Phunzilo la mtengo wa mkuyu wofota |
|
|
||
Yerusalemu, kacisi |
Atsutsa ulamulilo wake; fanizo la ana aŵili |
20:1-8 |
|
|||
Mafanizo: alimi akupha, phwando la cikwati |
20:9-19 |
|
||||
Ayankha mafunso onena za Mulungu na Kaisara, ciukililo, lamulo lalikulu |
20:20-40 |
|
||||
Afunsa khamu la anthu ngati Khristu ni mwana wa Davide |
20:41-44 |
|
||||
Tsoka alembi ndi Afarisi |
20:45-47 |
|
||||
Aona copeleka ca mkazi wamasiye |
|
21:1-4 |
|
|||
Phili la Maolivi |
Apeleka cizindikilo ca kubwela kwake kwa m’tsogolo |
21:5-38 |
|
|||
Mafanizo: anamwali 10, matalente, nkhosa na mbuzi |
|
|
|
|||
Nisani 12 (April 5-6, 2020) |
Yerusalemu |
Atsogoleli aciyuda akonza ciwembu cofuna kumupha |
22:1, 2 |
|
||
Yudasi alinganiza zom’peleka |
22:3-6 |
|
||||
Nisani 13 (April 6-7, 2020) |
Mu Yerusalemu na capafupi |
Akonzekela Pasika womaliza |
22:7-13 |
|
||
Nisani 14 (April 7-8, 2020) |
Yerusalemu |
Akudya mgonelo ndi atumwi ake |
22:14-18 |
|
||
Asambika mapazi a ophunzila ake |
|
|
|
13:1-20 |
||
Yesu azindikila Yudasi kukhala wom’peleka ndipo amuuza kuti acoke |
22:21-23 |
13:21-30 |
||||
Akhazikitsa Mgonelo wa Ambuye (1 Akor. 11:23-25) |
22:19, 20, 24-30 |
|
||||
Anenelatu za kukanidwa na Petulo ndi za kuthaŵa kwa atumwi |
22:31-38 |
13:31-38 |
||||
Alonjeza mthandizi; fanizo la mpesa weni-weni; apeleka lamulo lokondana; pemphelo lomaliza ndi atumwi |
|
|
|
14:1–17:26 |
||
Getsemane |
Nkhawa yaikulu m’munda; Kupelekedwa kwa Yesu na kumangidwa |
22:39-53 |
18:1-12 |
|||
Yerusalemu |
Afunsidwa ndi Anasi; ayesedwa na Kayafa, Sanihedrini; Petulo am’kana |
22:54-71 |
18:13-27 |
|||
Yudasi wom’peleka adzimangilila yekha (Mac. 1:18, 19) |
|
|
|
|||
Aonekela kwa Pilato, ndiyeno kwa Herode, ndipo am’bwezanso kwa Pilato |
23:1-12 |
18:28-38 |
||||
Pilato ayesa kum’masula koma Ayuda apempha kuti amasule Baraba; amupha pamtengo wozunzikilapo |
23:13-25 |
18:39–19:16 |
||||
(c. 3:00 masana.) |
Gologota |
Akufa pamtengo wozunzikilapo |
23:26-49 |
19:16-30 |
||
Yerusalemu |
Acotsa mtembo pamtengowo na kuuika m’manda |
23:50-56 |
19:31-42 |
|||
Nisani 15 (April 8-9, 2020) |
Yerusalemu |
Ansembe ndi Afarisi aika asilikali olondela manda na kutsekapo |
|
|
|
|
Nisani 16 (April 9-10, 2020) |
Yerusalemu na madela apafupi; Emau |
Yesu aukitsidwa; aonekela nthawi zisanu kwa ophunzila ake |
24:1-49 |
20:1-25 |
||
Pambuyo pa Nisani 16 |
Yerusalemu; Galileya |
Aonekelanso nthawi zambili kwa ophunzila ake (1 Akor. 15:5-7; Mac. 1:3-8); apeleka malangizo; awatuma kuti akapange ophunzila |
|
|
20:26–21:25 |