Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makambilano Acitsanzo

Makambilano Acitsanzo

●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi cifunilo ca Mulungu kwa anthu n’ciani?

Lemba: Gen. 1:28

Ulalo: Tidziŵa bwanji kuti Mulungu adzakwanilitsa cifunilo cake kwa anthu?

○●○ ULENDO WOBWELELAKO WOYAMBA

Funso: Tidziŵa bwanji kuti Mulungu adzakwanilitsa cifunilo cake kwa anthu?

Lemba: Yes. 55:11

Ulalo: Kodi umoyo udzakhala bwanji Mulungu akadzakwanilitsa cifunilo cake?

○○● ULENDO WOBWELELAKO WACIŴILI

Funso: Kodi umoyo udzakhala bwanji Mulungu akadzakwanilitsa cifunilo cake?

Lemba: Sal. 37:10, 11

Ulalo: Kodi tifunika kucita ciani kuti tikapindule na malonjezo a Mulungu?

KAMPENI YOMEMEZA ANTHU KU CIKUMBUTSO (March 14–April 7):

“Tabwela kudzakuitanilani ku cocitika capadela ca anthu mamiliyoni ambili. Cocitika cimeneci ni mwambo wokumbukila imfa ya Yesu.” Ndiyeno patsani munthuyo kapepa ka ciitanilo. “Kapepa ka ciitanilo aka kaonetsa nthawi na malo kumene cocitikaci cidzacitikile kwathu kuno. Tikuitanilaninso ku nkhani yapadela imene idzakambidwa pa wikendi yoti cikumbutso cicitika wiki yotsatila.”

Funso la Ulalo Akaonetsa Cidwi: N’cifukwa ciani Yesu anafa?