Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

April 13-19

GENESIS 31

April 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Yakobo na Labani Acita Pangano la Mtendele”: (10 min.)

    • Gen. 31:44-46—Yakobo na Labani anaunjika mulu wa miyala pamene anadyelapo cakudya ca pangano lawo (it-1 883 ¶1)

    • Gen. 31:47-50—Iwo anacha malowo Galeeda komanso Nsanja ya Mlonda (it-2 1172)

    • Gen. 31:51-53—Analonjezana kuti adzasungabe mtendele wawo

  • Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)

    • Gen. 31:19—N’ciani mwina cinapangitsa Rakele kuba aterafi a bambo ake? (it-2 1087-1088)

    • Gen. 31:41, 42—Kodi citsanzo ca Yakobo citiphunzitsa kuti tifunika kucita ciani ngati mabwana athu ni “ovuta kuwakondweletsa”? (1 Pet. 2:18; w13 3/15 21 ¶8)

    • Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?

  • Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 31:1-18 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

  • Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Pambuyo pake funsani omvetsela mafunso aya: Kodi mlongo walifotokoza bwanji lemba momveka bwino? Nanga wakamba ciani pofuna kukonzekeletsa mwininyumba za ulendo wobwelelako?

  • Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 4)

  • Ulendo Woyamba: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Kenako gaŵilani bulosha ya Uthenga Wabwino na kuyambitsa phunzilo la Baibo pa phunzilo 5. (th phunzilo 8)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

  • Nyimbo 77

  • Zofunikila za Mpingo: (15 min.)

  • Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 111 ¶1-9

  • Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)

  • Nyimbo 146 na Pemphelo