Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Cofunika Koposa kwa Ine N’ciani?

Kodi Cofunika Koposa kwa Ine N’ciani?

Yakobo anagwebana na mngelo kuti alandile cinthu cofunika kwambili, cimene ni dalitso la Yehova. (Gen. 32:24-31; Hoseya 12:3, 4) Nanga bwanji ife? Kodi timayesetsa kumvela Yehova kuti tilandile dalitso lake? Mwacitsanzo, kodi tingasankhe citi pakati pa kupita ku misonkhano ya mpingo kapena kukagwila nchito ya ovataimu? Ngati siticita kaso kupatsa Yehova nthawi yathu, mphamvu, na cuma cathu, iyenso adzatikhuthulila ‘madalitso oti tidzasoŵa powalandilila.’ (Mal. 3:10) Adzatitsogolela na kutiteteza ndipo adzatisamalila pa zosoŵa zathu.—Mat. 6:33; Aheb. 13:5

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI SUMIKANI MAGANIZO PA ZOLINGA ZAUZIMU, PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi mlongo anayesedwa bwanji na cinthu cimene amakonda?

  • Kodi nchito yathu ingakhale bwanji ciyeso kwa ise?

  • N’cifukwa ciani Timoteyo anafunika kupitiliza kudziikila zolinga ngakhale pamene anali wokhwima kuuzimu?—1 Tim. 4:16

  • Kodi cofunika koposa mu umoyo wanu n’ciani?

    Tingaonetse bwanji nchito “yofunika ngako” kwa ise?