Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 32-33

Kodi Mukulimbikila kuti Mupeze Madalitso?

Kodi Mukulimbikila kuti Mupeze Madalitso?

32:24-28

Kuti tilandile dalitso la Yehova, tifunika kulimbikila kuika zinthu za Ufumu patsogolo mu umoyo wathu. (1 Akor. 9:26, 27) Pamene titumikila Yehova, tiyenela kukhala na mzimu umene Yakobo anaonetsa polimbana na mngelo. Tingaonetse kuti tifuna dalitso la Yehova mwa . . .

  • Kukonzekela bwino misonkhano ya mpingo

  • Kutengako mbali nthawi zonse mu ulaliki

  • Kuyesetsa kuthandiza ena mumpingo

Olo kuti zinthu n’zovuta mu umoyo wanu, osaleka kupemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni. Komanso, limbikilani pom’tumikila ndipo adzakudalitsani.

Dzifunseni kuti: ‘Mu umoyo wanga, ni mbali ziti zimene nifunika kulimbikilapo kuti nilandile dalitso la Yehova?’