Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“Cotsani Milungu Yacilendo”

“Cotsani Milungu Yacilendo”

Yakobo anadziŵa kuti Yehova amafuna kuti tidzipeleke kwa iye yekha, ngakhale kuti Mulungu anali asanapeleke lamulo loletsa mafano. (Eks. 20:3-5) Conco, pamene Yehova anauza Yakobo kuti abwelele ku Beteli, iye anapempha onse amene anali naye kuti acotse mafano awo. Pambuyo pake, iye anataya mafanowo, kuphatikizapo masikiyo amene mwina anali kuvala monga zithumwa. (Gen. 35:1-4) Mosakayikila, Yehova anakondwela na zimene Yakobo anacita.

Masiku ano, kodi tingadzipeleke bwanji kwa Yehova yekha? Tingatelo mwa kupewa ciliconse cokhudzana na mafano kapena zamizimu. Izi zingaphatikizepo kutaya ciliconse cokhudza zamatsenga, komanso kupenda zosangalatsa zathu mosamala. Mwacitsanzo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi nimakonda kuŵelenga mabuku kapena kutamba mafilimu oonetsa zinthu monga vipuku, ziŵanda, kapena zamatsenga? Pa zosangalatsa zanga, kodi pali zina zoonetsa kuti kucita zamizimu, kulodza anthu ena kapena kuwatembelela kulibe vuto?’ Tiyenela kukhala kutali na ciliconse cimene Yehova amadana naco.—Sal. 97:10.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “TSUTSANI MDYELEKEZI,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi wophunzila Baibo dzina lake Palesa anakumana na vuto lanji mu umoyo wake?

  • N’cifukwa ciani n’canzelu kupempha thandizo kwa akulu pa nkhani zokhudza zamizimu?

  • Tsutsani Mdyelekezi, ndipo yandikilani Mulungu. —Yak. 4:7, 8

    Kodi anthu ofuna citetezo ca Yehova afunika kutaya zinthu ziti?

  • Kodi Palesa sanazengeleze kucita ciani?

  • Kudela lanu, ni njila zina ziti zimene mungatsatile kuti mupewe kuvutitsidwa na ziŵanda?