Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 34-35

Zotulukapo Zoopsa za Mayanjano Oipa

Zotulukapo Zoopsa za Mayanjano Oipa

34:1, 2, 7, 25

Ngati maneba athu, anzathu a kunchito kapena a kusukulu ali na makhalidwe abwino, kodi zitanthauza kuti angakhale mabwenzi abwino? N’ciani cingatithandize kudziŵa ngati munthu wina ni bwenzi labwino kapena ayi?

  • Kodi kukhala nawo paubwenzi kudzanithandiza kulimbitsa ubale wanga na Yehova?

  • Kodi zokamba zawo zimaonetsa kuti cofunika kwambili kwa iwo n’ciani?—Mat. 12:34

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mabwenzi anga amanilimbikitsa kukhala pa ubale wabwino na Yehova?’