August 1- 7
MASALIMO 87–91
Nyimbo 49 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khalanibe m’Malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba”: (Mph. 10)
Sal. 91:1, 2—‘Malo Acitetezo’ a Yehova amatithandiza kukhala otetezeka mwauzimu (w10 2/15-CN, tsa. 26-27 ndime 10-11)
Sal. 91:3—Mofanana ndi wosaka mbalame, Satana amafuna kutikola (w07 10/1-CN, tsa. 26-30 ndime 1-18)
Sal. 91:9-14—Yehova ndi malo athu acitetezo (w10 1/15-CN, tsa. 10-11 ndime 13-14; w01 11/15-CN, tsa. 19-20 ndime 13-19)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 89:34-37—Kodi mavesi amenewa akamba za pangano liti? Nanga Yehova anapeleka fanizo labwanji pofuna kuonetsa kuti panganolo n’lodalilika? (w14 10/15 tsa.10 ndime 14; w07 7/15-CN, tsa. 32 ndime 3-4)
Sal. 90:10, 12—Kodi tingaŵelengele bwanji “masiku athu kuti tikhale ndi mtima wanzelu”? (w06 7/15-CN, tsa. 13 ndime 4; w01 11/15-CN, tsa. 13 ndime 19)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal. 90:1-17
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani mavidiyo a maulaliki acitsanzo, ndipo kambilanani mfundo zake. Limbikitsani ofalitsa kukonza ulaliki wawo.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Nyimbo 141
Zosoŵa za pampingo: (Mph. 5)
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuthandiza Ophunzila Baibulo Kuti Adzipeleke ndi Kubatizika”: (Mph. 10.) Kukambilana. Funsani wofalitsa amene anathandizapo munthu wina kupita patsogolo mpaka kudzipeleka ndi kubatizika. Seŵenzetsani mafunso otsatilawa: Kodi wophunzila wanu munamuthandiza bwanji kuti ayambe kukonda kwambili Yehova? Nanga munamuthandiza bwanji kukwanilitsa zolinga zake zauzimu?
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 21 ndime 1-12
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 137 na Pemphelo