Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 87–91

Khalanibe m’Malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba

Khalanibe m’Malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba

“Malo Otetezeka” a Yehova amatithandiza kukhala otetezeka mwauzimu

91:1, 2, 9-14

  • Kuti tikhale m’malo otetezeka a Yehova, tifunika kudzipeleka ndi kubatizika

  • Amene sakhulupilila Mulungu, sawadziŵa malo otetezeka amenewa

  • Amene ali m’malo otetezeka a Yehova, salola kuti munthu wina kapena cinthu cina ciwalepheletse kukhulupilila Mulungu kapena kumukonda

“Wosaka mbalame” amachela misampha kuti atigwile

91:3

  • Mbalame n’zocenjela, ndipo n’zovuta kuzigwila

  • Wosaka mbalame amaona mmene mbalame zimacitila zinthu, ndipo amapeza njila yozigwilila

  • Satana, amene ndi “wosaka mbalame,” amaona zimene atumiki a Yehova amacita, ndipo amachela misampha kuti awaononge mwauzimu

Misampha inayi yowononga imene Satana amaseŵenzetsa:

  • Kuwopa Anthu

  • Kukonda Cuma

  • Zosangulutsa Zoipa

  • Mikangano