CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki —Kuthandiza Ophunzila Baibulo Kuti Adzipeleke ndi Kubatizika
CIFUKWA CAKE KULI KOFUNIKA: Kuti ophunzila Baibulo akhale pa ubwenzi wabwino na Yehova, afunika kudzipeleka ndi kubatizika. (1 Pet. 3:21) Ndiyeno akamacita zinthu mogwilizana ndi kudzipeleka kwawo, amakhala otetezeka mwauzimu. (Sal. 91:1, 2) Mkhiristu amadzipeleka kwa Yehova, osati kwa munthu wina, ku nchito, kapena ku gulu. Conco, ophunzila Baibulo afunika kukonda kwambili Mulungu ndi kumudziŵa bwino.—Aroma 14:7, 8.
MMENE TINGACITILE:
-
Pamene muphunzila nkhani iliyonse, muzikambilana mmene ikugwilizanilana ndi makhalidwe a Yehova. Mulimbikitseni kuti aziŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ndi kuti azipemphela kwa Yehova “mosalekeza.”—1 Ates. 5:17; Yak. 4:8
-
Limbikitsani wophunzila wanu kukhala na colinga codzipeleka ndi kubatizika. M’thandizeni kukhala na zolinga zina zing’onozing’ono, monga kuyankha pa misonkhano kapena kulalikila kwa anthu okhala nawo pafupi ndi anzake a ku nchito. Kumbukilani kuti Yehova sakakamiza aliyense kum’tumikila. Munthu afunika kudzipeleka mwa kufuna kwake.—Deut. 30:19, 20
-
Limbikitsani wophunzila wanu kusintha umoyo wake kuti akondweletse Yehova ndi kuti ayenelele ubatizo. (Miy. 27:11) Nthawi zina wophunzila Baibulo angakhale ndi makhalidwe ndi zizoloŵezi zoipa zimene zinazika mizu kwambili. Cotelo mungafunike kupitiliza kumuthandiza kuvula umunthu wakale ndi kuvala umunthu watsopano. (Aef. 4:22-24) Kambilanani naye nkhani zina za mu Nsanja ya Mlonda za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu”
-
Mfotokozeleni za cimwemwe cimene mwapeza cifukwa cotumikila Yehova.—Yes. 48:17, 18