Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

August 15-21

MASALIMO 102-105

August 15-21
  • Nyimbo 80 na Pemphelo

  • Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

  • Yehova Amadziŵa Kuti Ndife Fumbi: (Mph. 10)

    • Sal. 103:8-12—Yehova ali na cifundo, ndipo amatikhululukila ngati talapa (w13 6/15-CN, tsa. 20 ndime 14; w12 7/15-CN, tsa. 16 ndime 17)

    • Sal. 103:13, 14—Yehova amadziŵa zimene sitingakwanitse kucita (w15 4/15 26 ndime 8; w13 6/15-CN, tsa. 15 ndime 16)

    • Sal. 103:19, 22—Kuyamikila kukoma mtima kwa Yehova ndi cifundo cake, kuyenela kutilimbikitsa kucilikiza ulamulilo wake (w10 11/15-CN, tsa. 25 ndime 5; w07 12/1-CN, tsa. 21 ndime 1)

  • Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)

    • Sal. 102:12, 27—Kodi kuganizila ubwenzi wathu na Yehova kungatithandize bwanji tikavutika maganizo? (w14 3/1 tsa. 16 ndime 19-21)

    • Sal. 103:13—N’cifukwa ciani nthawi zina Yehova sayankha nthawi yomweyo mapemphelo ndi kutipatsa ciliconse cimene tifuna? (w15 4/15 tsa. 25 ndime 7)

    • Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?

    • Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?

  • Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal. 105:24-45

CITANI KHAMA PA ULALIKI

  • Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) g16. Na. 4 masa. 10-11—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.

  • Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) g16. Na 4 masa. 10-11—Yalani maziko a ulendo wina wobwelelako.

  • Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) bh masa. 164-166 ndime 3-4—Thandizani wophunzila kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’nkhani imeneyo.

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

  • Nyimbo 91

  • Musaiŵale Zimene Yehova Wakucitilani (Sal. 103:1-5): (Mph. 15) Kukambilana. Yambani mwa kutambitsa vidiyo ya pa jw.org yakuti N’nafika Poipidwa ndi Khalidwe Langa. (Pitani pa ZOKHUDZA IFE> ZIMENE TIMACITA.) Ndiyeno kambilanani mafunso awa: Kodi tili na zifukwa zabwanji zotamandila Yehova? Ni madalitso a mtsogolo ati amene tidzalandila kaamba ka kukoma mtima kwa Yehova?

  • Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 22 ndime 1-13

  • Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)

  • Nyimbo 131 na Pemphelo