MASALIMO 102-105
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |Yehova Amadziŵa Kuti Ndife Fumbi
Davide anaseŵenzetsa mafanizo pofotokoza cifundo ca Yehova.
-
103:11
Mofanana ndi mmene kumwamba kumene kuli nyenyezi kulili kutali na dziko lapansi, sitingathe kumvetsetsa bwino kukula kwa kukoma mtima kosatha kwa Yehova
-
103:12
Yehova amaika kutali kwambili macimo athu, monga mmene kum’maŵa kumatalikilana na kumadzulo.
-
103:13
Monga tate amene amacitila cifundo mwana wake amene wadzipweteka, Yehova amacitila cifundo anthu amene asweka mtima cifukwa ca macimo awo ndi kulapa