Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Phunzitsani Coonadi

Phunzitsani Coonadi

Kuyambila m’mwezi wa September, m’kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhiristu mudzayamba kukhala maulaliki a citsanzo wa mutu wakuti “Phunzitsani Coonadi.” Colinga cathu cizikhala kuphunzitsa anthu mfundo yomveka bwino ya coonadi ca m’Baibulo, pogwilitsila nchito funso na lemba.

Tikaona kuti munthu ali na cidwi, tingakulitse cidwi cake n’colinga cakuti tidzakambenso naye ulendo wina. Tingacite zimenezo mwa kumusiyila cofalitsa cinacake kapena kumuonetsa vidiyo ya pa jw.org. Tiziyesetsa kubwelelako mwamsanga kwa anthu amene takamba nawo kuti tikakulitse cidwi. Maulaliki acitsanzo amenewa ndiponso nkhani za ana a sukulu zidzakhala zocokela m’cigawo cakuti “Mfundo Zikulu” m’buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. M’cigawo cimeneci, muli mafunso na malemba amene angatithandize kucita maulendo obwelelako kapena kucititsa phunzilo mwa kuseŵenzetsa Baibulo cabe.

Pali njila imodzi cabe yotsogolela ku moyo. (Mat. 7:13, 14) Popeza kuti timakamba na anthu a zikhalidwe ndi zipembedzo zosiyanasiyana, tifunika kukamba mfundo za m’Baibulo zimene zingawacititse cidwi aliyense payekha. (1 Tim. 2:4) Tikadziŵa mfundo zambili za m’Baibulo ndi kukulitsa luso lathu ‘lophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a coonadi,’ tidzakhala na cimwemwe coculuka. Ndiponso tidzakwanitsa kuphunzitsa anthu coonadi ca m’Baibulo momveka bwino.—2 Tim. 2:15.