August 8- 14
MASALIMO 92-101
Nyimbo 28 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Amabala Zipatso Ngakhale ni Okalamba”: (Mph. 10)
Sal. 92:12—Wolungama amabala zipatso zauzimu (w07 9/15-CN, tsa. 32; w06 7/15-CN, tsa. 13 ndime 2)
Sal. 92:13, 14—Okalamba angabale zipatso zauzimu ngakhale atakhala na thanzi lofooka (w14 1/1, tsa. 26 ndime 17; w04 5/15-CN, tsa. 12 ndime 9-10)
Sal. 92:15—Okalamba angalimbikitse ena mwa kuwafotokozela zimene aona paumoyo wawo (w04 5/15-CN, masa. 12-14 ndime 13-18)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 99:6, 7—N’cifukwa ciani Mose, Aroni, na Samueli ni zitsanzo zabwino kwambili? (w15 7/15 tsa. 8 ndime 5)
Sal. 101:2—Kodi ‘kuyenda ndi mtima wosagaŵanika’ m’nyumba yathu kutanthauza ciani? (w05 11/1-CN, tsa. 24 ndime 14)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal. 95:1–96:13
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) g16. Na. 4 nkhani ya pacikuto—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) g16. Na. 4 nkhani ya pacikuto—Yalani maziko a ulendo wina wobwelelako.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) bh masa. 161-162 ndime 18-19—Thandizani wophunzila kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’nkhani imeneyo.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Nyimbo 90
Acikulile—Ndinu Ofunika Kwambili (Sal. 92:12-15): (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti: Acikulile—Ndinu Ofunika Kwambili. (Pitani pa jw.org, ndi kuona polemba kuti MABUKU > MAVIDIYO.) Ndiyeno pemphani omvela kuti akambe zimene aphunzilapo. Limbikitsani acikulile kuti aziuzako acicepele zinthu zimene iwo adziŵa. Limbikitsaninso acicepele kuti azifunsila kwa acikulile akafuna kupanga zosankha zofunika kwambili pa umoyo wawo.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 21 ndime 13-22, ndi kubwelelamo pa tsa. 186
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 29 na Pemphelo