UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO August 2018
Makambilano Acitsanzo
Makambilano otsatizana-tsatizana a mmene Baibo ilili yofunika masiku ano.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Muzionetsa Kuyamikila
Amene amafuna kukondweletsa Khristu ali na udindo kwa anthu onse, wowaonetsa cikondi na kuwayamikila, mosasamala kanthu za dziko lawo, mtundu wawo kapena cipembedzo cawo.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kumbukilani Mkazi wa Loti
Tingacite ciani kuti Mulungu asaleke kutiyanja monga mmene zinacitikila kwa mkazi wa Loti? Nanga bwanji ngati taona kuti zinthu zakuthupi zayamba kutidyela nthawi yocita zinthu zauzimu?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Phunzilamponi Kanthu pa Fanizo la Ndalama 10 za Mina
M’fanizo la Yesu la ndalama 10 za mina, kodi mbuye, akapolo, na ndalama ziimila ciani?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Webusaiti Yathu ya JW.ORG
Cofalitsa ciliconse cophunzitsila Baibo ca mu Thuboksi yathu, cimatsogolela anthu ku webusaiti yathu ya jw.org. Ngati tingaseŵenzetse webusaiti yathu, ulaliki wathu ungakhale wogwila mtima.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”
Posacedwa Yesu adzabwela kudzawononga oipa ndi kudzapulumutsa abwino. Tifunika kukonzekela mwauzimu kuti tikapulumuke.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Muzikhala Okonzeka Kukhululukila Ena
Yehova na Mwana wake amafufuza kuti aone ngati anthu amene acimwa ali na mtima wolapa n’colinga cakuti awacitile cifundo.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yesu Anafelanso M’bale Wako
Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka anthu ocimwa. Kodi abale na alongo amene ni opanda ungwilo ngati ise, tingawaonetse bwanji cikondi ngati cimene Khristu anationetsa?