Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yesu Anafelanso M’bale Wako

Yesu Anafelanso M’bale Wako

Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka anthu ocimwa. (Aroma 5:8) Mosakayikila, aliyense wa ise amayamikila kuti Yesu anationetsa cikondi mwa kutifela. Komabe, nthawi zina timaiŵala kuti Khristu anafelanso abale athu. Kodi abale na alongo amene ni opanda ungwilo ngati ise, tingawaonetse bwanji cikondi ngati cimene Khristu anationetsa? Ganizilani njila zitatu izi. Yoyamba, pa mabwenzi amene tili nawo kale tingawonjezelepo anthu a cikhalidwe cosiyana na cathu. (Aroma 15:7; 2 Akor. 6:12, 13) Yaciŵili, tiyenela kukhala osamala kuti tipewe kukamba kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. (Aroma 14:13-15) Yothela, ngati munthu wina watilakwila, tiyenela kumukhululukila mwamsanga. (Luka 17:3, 4; 23:34) Ngati tiyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu m’njila zitatuzi, Yehova adzapitiliza kudalitsa mpingo kuti ukhale wamtendele komanso wogwilizana.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALANI MUNTHU WABWINO KWAMBILI! NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Miki poyamba anali kuuona bwanji mpingo wake?

  • N’ciani cinamupangitsa kuyamba kukhala wokhumudwa?

  • Kodi citsanzo ca Yesu cinamuthandiza bwanji Miki kuyamba kuona zinthu moyenela? (Maliko 14:38)

  • Kodi Miyambo 19:11 ingatithandize bwanji kuyamba kuona Akhristu anzathu moyenela?