LUKA 17-18
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |Muzionetsa Kuyamikila
17:11-18
Kodi cocitika ici citiphunzitsa ciani pa nkhani ya kuyamikila?
-
Ciyamikilo cathu sicifunika cabe kuthela mu mtima koma tifunika kuciwonetsa
-
Kukamba mau oyamikila mocokela pansi pa mtima kumaonetsa kuti tili na cikondi cacikhristu, ndipo ni cizindikilo cakuti tili na aulemu
-
Amene amafuna kukondweletsa Khristu ali na udindo kwa anthu onse, wowaonetsa cikondi na kuwayamikila, mosasamala kanthu za dziko lawo, mtundu wawo kapena cipembedzo cawo.