UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Acinyamata—Khalani “Odzipeleka pa Nchito Zabwino”
M’kalata youzilidwa imene mtumwi Paulo analembela Tito, anakamba kuti anyamata, kuphatikizapo Tito, ayenela kuyesetsa kukhala “citsanzo pa nchito zabwino.” (Tito 2:6, 7) Kumapeto kwa caputa cimeneci, Paulo anaonetsa kuti anthu a Yehova amayeletsedwa kuti akhale “odzipeleka pa nchito zabwino.” (Tito 2:14) Imodzi mwa nchito zabwino zimenezo ni kulalikila komanso kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Ngati ndimwe wacinyamata, bwanji osaseŵenzetsa mphamvu zanu kuti mutumikile monga mpainiya wothandiza kapena wanthawi zonse?—Miy. 20:29.
Ngati mufuna kutumikila monga mpainiya, konzani ndandanda ya mmene mungacitile zinthu mu umoyo wanu. (Luka 14:28-30) Mwacitsanzo, kodi muzikapeza bwanji ndalama zokuthandizani pocita utumiki wanthawi zonse umenewu? Kodi muzikakwanitsa bwanji maola ofunikila? Pemphani Yehova kuti akuthandizeni pa nkhaniyi. (Sal. 37:5) Kambilanani na makolo anu zimene mwakonza. Mungakambilanenso na ena amene akukwanitsa kucita upainiya. Kenako citam’poni kanthu kuti mukwanilitse colinga canu. Mosakayikila, Yehova adzadalitsa khama lanu pamene mum’tumikila!
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI ACICEPELE OLEMEKEZA YEHOVA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Kodi ena anagonjetsa mavuto anji kuti atumikile monga apainiya? Nanga anawagonjetsa bwanji?
-
Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale apainiya a nthawi zonse?
-
N’cifukwa ciani kukhala na ndandanda ya ulaliki n’kofunika?
-
Kodi mpingo ungamulimbikitse bwanji mpainiya komanso kumuthandiza?
-
Kodi apainiya amapeza madalitso otani?