UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muziyanjana na Anthu Okonda Yehova
N’cifukwa ciani tifunika kuceza na anthu okonda Yehova? Cifukwa anthu amene timayanjana nawo angatilimbikitse kucita zinthu zabwino kapena zoipa. (Miy. 13:20) Mwacitsanzo, Mfumu Yehoasi anali “kucita zoyenela pamaso pa Yehova” pamene anali kuyanjana na Mkulu wa Ansembe, Yehoyada. (2 Mbiri 24:2) Koma pamene Yehoyada anamwalila, Yehoasi anapandukila Yehova cifukwa cogwilizana na anthu oipa. —2 Mbiri 24:17-19.
M’nthawi ya Akhristu oyambilila, mtumwi Paulo anayelekezela mpingo wacikhristu na “nyumba yaikulu,” ndipo anthu a mu mpingowo anawayelekezela na “ziwiya” za m’nyumbamo. Timakhalabe “ciwiya ca nchito yolemekezeka” ngati tipewa kuyanjana na aliyense amene amacita zinthu zokhumudwitsa Yehova, kaya akhale wacibale kapena wa mu mpingo. (2 Tim. 2:20, 21) Conco, tiyeni tipitilize kupanga ubwenzi na anthu amene amakonda Yehova, ndiponso amene angatilimbikitse kum’tumikila.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI PHUNZILANI KUPEWA MAKHALIDWE OIPA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
Kodi mosadziŵa tingayambe bwanji kuyanjana na anthu oipa?
-
Mu vidiyo imene tatamba, n’ciani cinathandiza Akhristu atatu kuleka kuyanjana na anthu oipa?
-
Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingakuthandizeni kusankha bwino anthu oyanjana nawo?