UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO December 2016
Maulaliki a Citsanzo
Maulaliki a citsanzo oseŵenzetsa pogaŵila Galamukani! ndi mfundo ya coonadi ca m’Baibo yokhudza cimene cimacititsa mavuto. Seŵenzetsani maulaliki a citsanzo pokonza ulaliki wanu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Tiyeni Tipite Kukakwela Phili la Yehova”
Mneneli Yesaya analosela kuti zida za nkhondo zidzakhala zolimila, kuonetsa kuti anthu a Yehova adzakhala pamtendele. (Yesaya 2:4)
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Afikeni pamtima ophunzila mwa kuseŵenzetsa buku lakuti, “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Buku la Cikondi ca Mulungu imathandiza ophunzila kudziŵa moseŵenzetsela mfundo za Mulungu mu umoyo wao wa tsiku na tsiku.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Mesiya Anakwanilitsa Ulosi
Mneneli Yesaya analosela kuti Mesiya adzalalikila ku Galileya. Yesu anakwanilitsa ulosi umenewu mwa kulalikila uthenga wabwino ku Galileya.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ine ndilipo! Nditumizeni.”
Tingatengele bwanji cikhulupililo na mzimu wofutsitsa wa Yesaya? Tengelani citsanzo ca banja limene linapita kukatumikila kosoŵa.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Dziko Lapansi Lidzadzala na Ŵanthu Odziŵa Yehova
Kodi ulosi wa Yesaya wokamba za paradaiso unakwanitsika bwanji kale, masiku ano na mtsogolo?
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Maphunzilo Aumulungu Amagonjetsa Tsankho
Amuna aŵili amene anali paudani anakhala paubale wauzimu—umboni wakuti maphunzilo aumulungu ali na mphamvu yotigwilizanitsa.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kuseŵenzetsa Mphamvu Mwadyela Kumatayitsa Udindo
Kodi Sebina anafunikila kuseŵenzetsa bwanji udindo wake? N’cifukwa ciani Yehova anaika Eliyakimu pa udindo wa Sebina?