Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 6-10

Mesiya Anakwanilitsa Ulosi

Mesiya Anakwanilitsa Ulosi

Zaka zambili Yesu akalibe kubadwa, Yesaya analosela kuti Mesiya akayamba kulalikila “m’cigawo ca Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.” Yesu anakwanilitsa ulosiwu pamene anali kuyenda m’Galileya monse kulalikila uthenga wabwino.—Yes. 9:1, 2.

  • Anacita cozizwitsa coyamba—Yoh. 2:1-11 (ku Kana)

  • Anasankha atumwi ake—Maliko 3:13, 14 (pafupi na Kaperenao)

  • Analalikila pa phili—Mat. 5:1–7:27 (pafupi na Kaperenao)

  • Anaukitsa mwana mmodzi yekha wa mayi wamasiye—Luka 7:11-17 (ku Naini)

  • Anaonekela kwa ophunzila ake 500 pambuyo poukitsidwa—1 Akor. 15:6 (ku Galileya)