Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Afikeni pamtima ophunzila mwa kuseŵenzetsa buku lakuti, “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”

Afikeni pamtima ophunzila mwa kuseŵenzetsa buku lakuti, “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”

CIFUKWA CAKE KULI KOFUNIKA: Anthu afunika kuphunzila miyezo ya Yehova na kuyamba kuitsatila kuti azimulambila movomelezeka. (Yes. 2:3, 4) Buku yakuti “Khalanibe m’Cikondi,” imene ni buku yaciŵili yophunzila, imathandiza ophunzila Baibo kudziŵa mmene angaseŵenzetsele mfundo za umulungu mu umoyo wawo. (Aheb. 5:14) Poŵaphunzitsa, tiyenela kuyesetsa kuwafika pamtima kuti atunthike kusintha umoyo wawo.—Aroma 6:17.

MMENE TINGACITILE

  • Konzekelani bwino, poganizilanso zosoŵa za wophunzila wanu. Konzani mafunso amene adzakuthandizani kudziŵa maganizo ake na mmene akuionela nkhaniyo.—Miy. 20:5; be tsa. 259

  • Seŵenzetsani mabokosi onse amene ali m’bukuli kuti muthandize wophunzila Baibo kuona ubwino woseŵenzetsa mfundo za m’Baibo

  • Thandizani wophunzila Baibo kuti azilingalila bwino pankhani zokhudza cikumbumtima, koma osamupangila zosankha.—Agal. 6:5

  • • Mosamala, onani ngati wophunzila wanu afunikila thandizo pa kugwilitsila nchito mfundo zina za m’Baibo. Muthandizeni kuona kuti afunika kusintha cifukwa ca cikondi cake pa Yehova.—Miy. 27:11; Yoh. 14:31