YESAYA 1-5
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |“Tiyeni Tipite Kukakwela Phili la Yehova”
2:2, 3
“Masiku otsiliza” |
Ni nthawi ino imene tikhalamo |
“Phili la nyumba ya Yehova” |
Kulambila Yehova kokwezeka ndi koyela |
“Mitundu yonse idzakhamukila kumeneko” |
Amene amalambila m’njila yoyela amasonkhana mu umodzi |
“Bwelani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwela phili la Yehova” |
Olambila oona amaitana anthu ena kuti azilambila nawo pamodzi |
“Iye akatiphunzitsa njila zake, ndipo ife tidzayenda m’njila zakezo.” |
Kupitila m’Mau ake, Yehova amatiphunzitsa na kutithandiza kuti tiziyenda m’njila zake |
2:4
“Sadzaphunzilanso nkhondo” |
Yesaya anafotokoza kuti zida za nkhondo zidzasinthiwa kukhala zolimila, kuonetsa kuti anthu a Yehova adzakhala amtendele. Kodi zida zimenezi zinali ciani m’nthawi ya Yesaya? |
‘Malupanga akhala makasu a pulawo’ |
1 Pulawo inali cida cofala cogawulila nthaka. Mapulawo ena anali ansimbi.—1 Sam. 13:20 |
‘Mikondo ikhala zida zosadzila mitengo’ |
2 Cida cosadzila mitengo cinali cimpeni copindika monga comwetela udzu. Cinali codulila mpesa.—Yes. 18:5 |