UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO December 2018
Makambilano Acitsanzo
Makambilano otsatizana-tsatizana ofotokoza colinga ca moyo na lonjezo la Mulungu la m’tsogolo.
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Wozunza Akhristu Mwankhaza Akhala Mlaliki Wokangalika
Ngati mumaphunzila Baibo koma simunabatizike, kodi mudzatengela citsanzo ca Saulo mwa kucitapo kanthu mwamsanga pa zimene mumaphunzila?
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Paulo na Baranaba Apanga Ophunzila Kumadela Akutali
Ngakhale kuti Paulo na Baranaba anatsutsidwa mwamphamvu, anacita khama kuthandiza anthu ofatsa kukhala Akhristu.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuthandiza Anthu a “Maganizo Abwino” Kukhala Ophunzila
Kodi timagwila bwanji nchito na Yehova popanga ophunzila?
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Cigamulo Cozikidwa pa Mawu a Mulungu
Tiphunzilapo ciani pa mmene nkhaniyi anaisamalila?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muziimba Mosangalala Nyimbo Zotamanda Yehova
Kodi kuimba nyimbo za Ufumu kumatikhudza bwanji?
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Tengelani Citsanzo ca Mtumwi Paulo Polalikila na Kuphunzitsa
Tingatengele bwanji citsanzo ca mtumwi Paulo pocita ulaliki wathu?
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mukhale Chelu ndi Kuyang’anila Gulu Lonse la Nkhosa”
Akulu amadyetsa nkhosa, kuziteteza na kuzisamalila. Amakumbukila kuti nkhosa iliyonse inagulidwa na magazi a mtengo wapatali a Khristu.