December 31–January 6
MACHITIDWE 19-20
Nyimbo 103 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mukhale Chelu ndi Kuyang’anila Gulu Lonse la Nkhosa”: (10 min.)
Mac. 20:28—Akulu amaŵeta mpingo wa Mulungu (w11 6/15 mape. 20-21 pala. 5)
Mac. 20:31—Pakakhala pofunikila, Akulu amapeleka cithandizo “usana ndi usiku” (w13 2/1 peji 31 pala. 15)
Mac. 20:35—Akulu afunika kukhala na mzimu wodzimana (bt peji 172 pala. 20)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mac. 19:9—Kodi Paulo anatipatsa citsanzo cotani pa nkhani yocita khama, ndiponso kusintha njila zolalikilila? (bt peji 161 pala. 11)
Mac. 19:19—Kodi Akhristu a ku Efeso anapeleka citsanzo cotani cimene tingatengele? (bt mape. 162-163 pala. 15)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mac. 19:1-20
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kubwelelako Kaciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Gaŵilani mwininyumba kakhadi kongenela pa webusaiti ya JW.ORG.
Kubwelelako Kacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Sankhani mwekha lemba na funso lokakambilana ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) jl phunzilo 15
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Phunzitsani Anyamata Amene Akukalamila Maudindo: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo imeneyi. Ndiyeno yankhani mafunso aya: Ni udindo wofunika kwambili uti umene akulu ali nawo mu mpingo? (Mac. 20:28) N’cifukwa ciani akulu afunika kupitiliza kuphunzitsa ena? Kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca mmene Yesu anali kuphunzitsila atumwi ake? Kodi abale amene a akuphunzitsidwa afunika kukhala na khalidwe lotani? (Mac. 20:35; 1 Tim. 3:1) Nanga kodi akulu angawaphunzitse zotani abale amenewa? Kodi akulu ayenela kuwaona bwanji abale amene iwo akuphunzitsa?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 48
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 118 na Pemphelo