UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Khalani Okonzeka Kusintha Ulaliki
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Odzozedwa komanso a nkhosa zina amaitanila anthu kuti “amwe madzi a moyo kwaulele.” (Chiv. 22:17) Madzi ophiphilitsila amenewa aimila zinthu zonse zimene Yehova wapeleka kuti zipulumutse anthu omvela ku ucimo na imfa. Kuti tithandize anthu kucoka ku miyambo yawo na zikhulupililo za cipembedzo cawo, tifunika kulalikila “uthenga wabwino” m’njila yakuti uziwafika pamtima.—Chiv. 14:6
MMENE TINGACITILE:
-
Sankhani nkhani na lemba limene lingafike pamtima anthu m’gawo lanu. Mungasankhe makambilano acitsanzo kapena nkhani ina imene munagwilitsapo nchito, imene inali na zotulukapo zabwino. Kodi anthu amacita cidwi na nkhani ziti ndiponso malemba ati? Kodi pali nkhani ya pa nyuzi imene anthu ambili akukambapo? Ni nkhani ziti zimene zingakope akazi kapena amuna?
-
Pokambilana na anthu, muziwapatsa moni komanso muzicita zinthu mogwilizana na cikhalidwe ca kwanuko.—2 Akor. 6:3, 4
-
Zidziŵeni bwino zofalitsa na mavidiyo a mu Thuboksi yathu Yophunzitsila kuti mugaŵaleko munthu amene angaonetse cidwi
-
Citani daunilodi zofalitsa za m’citundu ca anthu amene mungakumane nawo m’gawo lanu.
-
Sinthani ulaliki wanu kuti ukhale wogwilizana na zosoŵa za mwininyumba. (1 Akor. 9:19-23) Mwacitsanzo, kodi mungakambe ciani ngati mwadziŵa kuti posacedwa mwininyumba anataikilidwa wokondedwa wake mu imfa?
TAMBITSANI VIDIYO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Kodi wofalitsa anayamba kukambilana nkhani yanji na mwininyumba?
-
Kodi mwininyumba anakumana na mavuto otani mu umoyo wake?
-
Ni lemba liti limene likanagwilizana bwino na cocitikaco? Nanga n’cifukwa ciani?
-
Mungasinthe bwanji ulaliki wanu kuti ukhale wokopa kwa anthu a m’gawo lanu?