UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Dzikolo ‘Linameza Mtsinje’
Pa nthawi zosiyana-siyana m’mbili ya anthu, olamulila akhala akuthandiza anthu a Yehova. (Ezara 6:1-12; Esitere 8:10-13) Ngakhale masiku ano, timaona kuti “dziko” kapena kuti olamulila a dziko amaganizo abwino, amameza “mtsinje” wa cizunzo woyambitsidwa na “cinjoka,” cimene ni Satana Mdyelekezi. (Chiv. 12:16) Yehova, “Mulungu amene amatipulumutsa,” nthawi zina angaseŵenzetse olamulila kuti athandize anthu ake.—Sal. 68:20; Miy. 21:1.
Nanga bwanji ngati mwamangidwa cifukwa ca cikhulupililo canu? Musakayikile kuti Yehova akuona zimene zikukucitikilani. (Gen. 39:21-23; Sal. 105:17-20) Dziŵani kuti mudzadalitsidwa cifukwa ca cikhulupililo canu, komanso kuti kukhulupilika kwanu kumalimbikitsa abale padziko lonse.—Afil. 1:12-14; Chiv. 2:10.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI ABALE KU KOREA ATULUTSIDWA M’NDENDE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
N’cifukwa ciani kwa zaka zambili abale athu masauzande ku South Korea anali kumangidwa?
-
Ni ziweluzo zotani zimene khoti linapeleka kuti ena mwa abale athu amasulidwe mwamsanga?
-
Tingawathandize bwanji abale athu pa dziko lonse amene amangidwa cifukwa ca cikhulupililo cawo?
-
Kodi ufulu umene tili nawo tingauseŵenzetse bwanji?
-
N’ndani amapangitsa kuti tiwine milandu ku khoti?