CHIVUMBULUTSO 10-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |‘Mboni Ziŵili’ Zinaphedwa, Kenako Zinakhalanso na Moyo
11:3-11
-
‘Mboni Ziŵili’: Kagulu ka abale odzozedwa amene anali kutsogolela pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914
-
Kuphedwa: Pambuyo polalikila kwa zaka zitatu na hafu ‘atavala ziguduli,’ iwo anaphedwa pamene anamangiwa, cakuti sanathenso kugwila nchito zawo
-
Kukhalanso na moyo: Cakumapeto kwa zaka zitatu na hafu zophiphilitsila, iwo anakhalanso na moyo pamene anatulutsidwa m’ndende na kuyambanso kutsogolela pa nchito yolalikila