LEVITIKO 12-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Phunzilamponi Kanthu pa Malamulo Okhudza Nthenda ya Khate
13:4, 5, 45, 46, 52, 57
Kodi mfundo zimene panazikidwa malamulo okhudza nthenda ya khate zitiphunzitsa ciani pa nkhani yoteteza umoyo wathu wauzimu?
-
Yehova anaphunzitsa ansembe mmene angaidziŵile mwamsanga nthenda ya khate. Abusa acikhristu masiku ano amacita cangu kuthandiza anthu amene afunika thandizo lauzimu.—Yak. 5:14, 15
-
Aisiraeli anali kuwononga cinthu ciliconse cimene khate lafalikilapo, pofuna kuti lisapitilize kufalikila. Nawonso Akhristu afunika kulolela kuleka kapena kudzimana zinthu zina m’malo molola kuti zinthuzo ziwagwetsele m’chimo. (Mat. 18:8, 9) Zinthu zimenezo zingaphatikizepo zizoloŵezi zoipa, mayanjano, kapena zosangalatsa zoipa
Kodi munthu angaonetse bwanji kuti afunitsitsa kulandila thandizo locokela kwa Yehova?